languagesoftware.net - which is the best language course or software - compare

Learn French with Frantastique

Babel

The Tower of Babel (Genesis 11: 1-9)

Chicheŵa (Chichewa)

  1. Tsopano padziko lonse lapansi panali chilankhulo chimodzi ndipo anthu anali kugwiritsa ntchito mawu ofanana.
  2. Pamene anthuwo analowera chakum'mawa, anapeza chigwa m'dera la Sinara n'kukhazikika kumeneko.
  3. Kenako anauzana kuti: "Tiyeni tiumbe njerwa tiziotche." Atatero, anayamba kumanga ndi njerwa, n'kumagwiritsa ntchito phula ngati matope omangira.
  4. Ndiyeno anati: "Tiyeni timange mzinda wathuwathu, ndipo nsanja yake ikafike m'mwamba mwenimweni. Tikatero tidzipangira dzina loti titchuke nalo, ndipo sitibalalikana padziko lonse lapansi."
  5. Kenako, Yehova anatsikirako kukaona mzinda ndi nsanja imene ana a anthu anali kumanga.
  6. Pamenepo Yehova anati: "Taonani! Izi n'zimene anthuwa ayamba kuchita popeza ndi amodzi ndipo onse ali ndi chilankhulo chimodzi. Mmene zililimu, angathe kuchita chilichonse chimene akuganiza.
  7. Choncho, tiyeni tipiteko kuti tikasokoneze chilankhulo chawo, kuti asamamvane polankhula."
  8. Motero, Yehova anawabalalitsa pamalopo, kuti afalikire padziko lonse lapansi. Zitatero, iwo anasiya pang'onopang'ono kumanga mzindawo.
  9. Mzindawo unatchedwa Babele, chifukwa kumeneko, Yehova anasokoneza chilankhulo cha anthu onse, ndipo Yehova anabalalitsira anthuwo padziko lonse lapansi.

From: Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika


Cheap Web Hosting